Cart 0
Sindikhulupirira Kuti Ndine! Mungadziwe bwanji mmene muonekera opanda kalilole? (Nyanja)

Sindikhulupirira Kuti Ndine! Mungadziwe bwanji mmene muonekera opanda kalilole? (Nyanja)

$0.00

NDI CINTHU COSEKETSA KUTI TIKHOZA KUONA bwino nkhope za anthu ena, koma nkhope zathu zathu sitingathe kuziona. Kalilole atithandiza kuona nkhope zathu. Poyangana pa kalilole tingathe kudziona tokha bwino. Kalilole atithandiza kuona zimene sizili bwino ndi kuzikonza.

Kalilole atithandiza kuona mmene tilili kunja kwa thupi lathu. Pali kalilole wina amene ationetsa za mkati mwathu. Kodi kalilole ameneyo ndi uti? Kalilole ameneyo ndi Buku Lopatulika.

Amene sali mkristu powerenga Baibulo, kapena pomvetsela pa zimene Baibulo liphunzitsa adzaona cithunzi ca moyo wace.

“Mkwiyo, dumbo, mau oipa, bodza.” Akolose 3:8-9. “Cilakolako coipa, cisiliro, kulankhula zopusa. Cifukwa ca izi zomwe ukudza mkwiyo wa Mulungu pa ana akusamvera.” Akolose 3:5-6. “Opanda Kristu, opanda ciyembekezo, opanda Mulungu m’dziko lapansi.” Aefeso 2:12.

Kodi muli kunena, “Sindikhulupirira kuti ndine?” Ngati simuli mkristu mudziwa kuti ndi cithunzithunzi coona ca mtima wanu. Kalilole anena zoona. Cikumbu-mtima canu cinena, “Inde, cimeneco ndi coona ca ine.”

Koma pamene taima patsogolo pa kalilole ndipo taona mmene mitima yathu ilili, tsono Baibulo litiimitsa pamaso pa Munthu. Iye ali wokonda, wanzeru, ndi wamphamvu. Iye alankhula nafe nati, “Ndidziwa mtima wako uli kudwala, koma ndingathe kuukonza. Ndidziwa mtima wako uli wodetsa koma ndingathe kuuyeretsa konse konse. Ndidziwa kuti wacimwa koma ndakufera kut ukhululukidwe. Bwera kwa ine. Ndidzakulandira iwe ndi kukusunga iwe.”

YESU ADZAKUKHULULUKIRA.
“Ngati tibvomereza macimo athu, ali wokhulupirika ndi wolungama Iye kuti atikhululukire macimo athu.”1 Yohane 1:9.

ADZAYERETSA MTIMA WAKO.
“Mwazi wa Yesu Mwana wace utisambitsa kuticotsera ucimo wonse.” I Yohane 1:7.

ADZAKULIMBIKITSA IWE.
“Ndikhoza zonse mwa Iye wondipatsa mphamvuyo’” Afilipi 4:13.

ADZAKUPATSA IWE MTENDERE.
“Ndipo Ambuye wa mtendere yekha atipatse ife mtendere nthawi zonse.” 2 Atesalonika 3:16.

ADZAKUPATSA CIMWEMWE.
“Kuti cimwemwe canga cikhale mwa inu ndi kut cimwemwe canu cidzale.” Yohane 15:11. Palibe wina angathe kucita mu mtima mwanu monga Ambuye Yesu Kristu. Muloleni alowe mu mtima mwanu lero.

Yamikani Mulungu Cifukwa Ca Baibulo.
Litisonyeza Zimine Zili Zocimwa M’mitima Mwathu.
Litsonyeza Za Mmodzi Amene Angathe Kukonza Zonse.
Ambuya Yesu Kristu.
Kodi Iye Ndi Ambuye Wanu Ndi Mpulumutsi Wanu?More from this collection