Cart 0
Njira yopita ku Moyo (Chichewa)

Njira yopita ku Moyo (Chichewa)

$0.00

KODI NDI INU AMENE MULI PA THANTHWE LA IMFA?
Munthu amene ali pa thanthweyo akuyimilira mtundu uliwonse wa anthu. Vuto lake ndi tchimo. “Pakuti onse anachimwa naperewera pa ulemerero wa Mulungu” Aroma 3:23. Tchimo labweretsa imfa ya uzimu pa munthu. Baibulo limanena kuti “Pakuti mphoto yache ya uchimo ndi imfa...” Aroma 6:23. “...chotero imfa inafikira anthu onse chifukwa kuti onse anachimwa” Aroma 5:12b. Imeneyi si imfa ya kuthupi ayi koma imfa ya uzimu. Izi zitanthauza kuti moyo wosiyanitsidwa ndi Mulungu ndi “wokufa ndi zolakwa ndi zochimwa” Aefeso 2:1. Kodi kapena ndi inu amene muli pa thanthwe la imfa? Ngati simunalandirebe Yesu Khristu kukhala mpulumutsi wanu, muli pa mlandu wa imfa chifukwa Baibulo limanena kuti “...iye wosakhala ndi mwana wa Mulungu alibe moyo” 1 Yohane 5:12b. Mwina mukhoza kunena kuti “Sindifunanso kukhala mu imfa koma palibe mlatho woolokera kuchokera ku thanthwe la imfa kupita ku thanthwe la moyo. Kodi ndingadutse bwanji kuchokera ku imfa kupita ku moyo?”

MLATHO WA NTCHITO ZABWINO, UBATIZO NDI UMEMBALA WA MPINGO
Poyang’ana njira yofuna kudutsa kuchokera ku thanthwe la imfa kupita ku thanthwe la moyo, musalakwitse monga m’mene amachitira anthu ambiri ponena kuti “Ndidzapulumutsidwa chifukwa cha ntchito zanga zabwino.” Popeza Baibulo limanena kuti “Pakuti muli opulumutsidwa ndi chisomo chakuchita mwa chikhulupiliro, ndipo ichi chosachokera kwa inu; chiri mphatso ya Mulungu; chosachokera ku ntchito; kuti asadzitamandire munthu aliyense” Aefeso 2:8-9. Mlatho wa ntchito zabwino siwokwanira kuchokera ku imfa kupita ku moyo. Ndifunanso ndikuchenjezeni kuti simuyenera kulakwitsa monga m’mene amachitira anthu ena ponena kuti “ Ine ndinabatizidwa ndipo ndine membala wa mpingo nanga china chatsala ndi chiyani choti Mulungu akhoza kundifunsa?” Baibulo limanena kuti, “Ngati munthu sabadwa mwatsopano sangathe kuona ufumu wa Mulungu” Yohane 3:3. Yesu analankhula zimenezi kwa Myuda wina wotchedwa Nikodemo. Nikodemo anali munthu wa chipembedzo; mkulu wa Ayuda komanso membala wa sunagoge, koma moyo wake wa chipembedzo sukanatha kumuchotsa ku imfa ndi kupita ku moyo. Mlatho wa ubatizo ndi umembala wa mpingo ndi waufupi kwambiri.

MULUNGU ANAPEREKA NJIRA
Mulungu anadziwa kuti munthu sangathe kupeza njira yochokera ku imfa kupita ku moyo. Popeza Iye anamlenga munthu ndipo anapitirizabe kumukonda, Mulungu mwini wake anapeza njira. Yesu ndiye njira yochokera ku imfa kupita ku moyo. Iye anati, “Ine ndine njira...palibe munthu adza kwa Atate koma mwa Ine” Yohane 14:6. Mwina mutha kufunsa kuti kodi Yesu angakhale bwanji njira? Taonani, Mulungu anati; “Moyo wochimwawo ndiwo udzafa” Ezekieli18:4b. Popeza Mulungu ndi chikondi, Iye sanafune kuti munthu aweruzidwe ndi kupita ku gahena wamuyaya. Nanga Iye anamusunga munthu bwanji ndi kukhalabe wokhulupirika ku mau ake, popeza Iye ananena kuti munthu wochimwa adzafa? Pamenepa ndi pamene Mulungu anawonetsa chikondi chake kwa munthu. Iye anatumiza Yesu kufa pa mtanda m’malo mwa munthu. “Pakuti Mulungu anakonda dziko lapansi, kotero kuti anapatsa mwana wake wobadwa yekha kuti yense wokhulupilira Iye asatayike, koma akhale nawo moyo wosatha” Yohane 3:16. Ichi ndi chifukwa chake Yesu ali njira yochokera ku imfa kupita ku moyo; Iye anasenza chilango chako. Ngati iwe ungamulandire Iye kuti akhale mpulumutsi wa moyo wako pamenepo machimo ako adzakhululukidwa ndipo udzalandira moyo wosatha. “Iye wakukhala ndi mwana ali nao moyo” 1Yohane 5:12a.

MUKHONZA KUCHOKA KU IMFA KUPITA KU MOYO
Yesu anati; “Iye wakumva mau anga ndi kukhulupilira Iye amene anandituma Ine, ali nao moyo wosatha ndipo salowa mkuweruza; koma wachokera ku imfa nalowa m’moyo” Yohane 5:24.

GAWO LANU
1. MUYENERA KUMVA MAU A MULUNGU (Baibulo). Baibulo limatiuza kuti ife ndi ochimwa ndipo tiyenera kufa. Limatiuzanso kuti Yesu anafa chifukwa cha machimo athu.
2. MUYENERA KULAPA MACHIMO ANU. “Chifukwa chake lapani, bwererani kuti afafanizidwe machimo anu...” Machitidwe 3:19a.
3. MUYENERA KUKHULUPILIRA MWA KHRISTU. “Ukhulupilire Ambuye Yesu Khristu ndipo udzapulumuka” Machitidwe 16:31. Kukhulupilira kumatanthauza kuzindikira kuti Khristu anafa chifukwa cha zochimwa zanu. Zikutanthauzanso kubwera kwa Yesu Khristu ndi zochimwa zanu zonse ndi kumupempha Iye kuti akupulumutseni. Komanso zikutanthauza kumukhulupilira Iye kuti akulandirani ndi kukupulumutsani.

GAWO LA MULUNGU
1. IYE ADZAKHULULUKIRA MACHIMO ANU.
2. IYE ADZAKUPATSANI MOYO WOSATHA.

Kodi mwachoka ku imfa kupita ku moyo?
Ngati sichoncho, chitani chimenechi tsopano! Chifukwa mwina mawa ndi patali kwambiri. Pakalipano mupempheni Yesu kuti alowe mu mtima mwanu ndi kukupulumutsani. Nthawi yomweyo mwangochita chimenechi, mudzachoka ku imfa ndi kulowa ku moyo.- John C. RatzlaffMore from this collection