Cart 0
Cenjerani !… 	...Cenjerani ! (Nyanja)

Cenjerani !… ...Cenjerani ! (Nyanja)

$0.00

M’DZIKO LATHU lino kumadera kumene kuli zirombo, mbusa ayenera kuweta nkhosa zace mosamala kuti nkhosa pamodzi ndi ana a nkhosa zace zisagwe m’zobvuta. Mbusa wabwino aweta nkhosa zace mosamalitsadi. Safuna kuti imodzi itayike. Ndi zamwai nkhosa zimene zili ndi mbusa wabwino. Iye apulumutsa moyo wao nazichinjiliza kwa adani ao ndipo kuti zosawo zao zonse azikwanilitsa.

Ifenso tifuna mbusa, mbusa wa miyoyo yathu ya uzimu. Cifukwa ninji?

1. Popeza pafupi ndi ife, pali adani amene afuna kutiononga. Mdani mmodzi wamkulu walowa kale m’mitima yathu ndipo aticititsa ife zoipa. Dzina lace ndi Satana. Saoneka, koma agwiritsa nchito m’mitima yathu. Satikonda, safuna konse kuticititsa cabwino ciloconse. Ndiye mdani weniweni. Iye adziwa kuti sadzapita kwina koma ku Gahena, ndipo afuna kutikankhira ife pamodzi naye komweko. ‘Mdierekezi monga mkango wobuma ayendayenda ndi kufunafuna wina akamlikwire’ -I Petro 5:8.

2. Popeza sitingathe kudzisunga tokha. Tiri ngati nkhosa, ndipo titaya njira yoyenera ndikugwa m’zobvuta zosiyanasiyana. Tiyenera kukhala ndi wina wanzeru, wamphamvu ndi wacikondi, kuticenjeza pa zoopsa, ndikutisunga panjira yoyenera ndikuti akhale bwenzi lathu labwino. Sicapafupi kupeza njira yeniyeni m’moyo uno. Tikhoza kulakwa tikapanda mtsogoleri. ‘Tonse tasocera ngati nkhosa’ Yesaya 53:6.

Yesu Kristu ndi Mbusa woona ndi wabwino yekhayo amene ali Mwana wa Mulungu. Pamene chimo linalowa pansi pano, linamwaza gulu la nkhosa la Mulungu monga ngati mkango womwaza gulu la nkhoza. Ndipo chimo silikadalola kuti ife tibwererenso kwa Mulungu. Koma Mulungu anatikonda ife ndipo anatumiza mwana wace, Ambuye Yesu, kutipulumutsa ife. Yesu satibalalitsa ife ai. Atisonkhanitsa ife kwa Iye mwini. Iye ndi mbusa watiitanira ife kwa Iye mwini ndikutibwezanso kwa Mulungu.

Iye mwini watsimikiza yekha kuti ndiye mbusa wabwino. Bwanji ?

1. Iye anatsikira pansi pano kucokera kumwamba kuti atipatse thandizo limene ife tilifuna. Mbusa ayenera kukhala komwe kuli nkhosa. Sangakhale wosangalala m’nyumba yace ngati afuna kukhala mbusa weniweni kwa nkhoza zace. Yesu anasiya zokondweretsa zonse za M’mwamba. Anafika pansi pano, ndipo anali wosowa ndi wanjala ndi wotopa, anasauka nazo zomwezi zakuti ife tisauka nazo kuti akhale mbusa weniweni kwa ife. ‘Iye anatsika kucokera kumwamba’ - Yohane 3:13. ‘Kristu adamva zowawa m’thupi - 1 Petro 4:1.

2. Anapereka moyo wace cifukwa ca ife. Mwa macimo athu ife tinagwa m’ngongole yoopsa kwa Mulungu mmene sitikadakhoza kubwezera; motero Iye anatuma mwana wace wobadwa yekha kubweza ngongoleyo mwakutifera ife pa mtanda. Yesu anabvomera kucita ici ndi mtima wonse cifukwa atikonda ife. Mbusa wabwino ayenera kuona zobvuta kupulumutsa nkhosa zace. Yesu anapereka moyo wace kutipulumutsa ife. Kodi alipo wina amene mumdziwa amene anatsimikiza kukhala mbusa wabwino kwa inu monga m’mene anacitira Yesu? ‘Mbusa wabwino ataya moyo wace cifukwa ca nkhosa’ - Yohane 10:11.

3. Pamene ngongole yathu inaperekedwa kotheratu, Mulungu anamuukitsa Yesu kwa aKufa. M’moyo wace woukitsidwa watsopano, atisamalirabe ife. Satiiwala ife ai, atikonda. Pamene anabwerera kumwamba, Anatumiza Mzimu Woyera kudziko lapansi kukhala m’mitima ya anthu onse amene amucha Iye mpulumutsi wao. ‘Iye asamalira inu’ - 1 Petro 5:7.

Kodi monga mukuti Yesu si mbusa wanu? Ngati mutero cifukwa cace ndico kuti inuyo simufika kwa Iye pamene Iye akuitanani. Mukakalata aka mulikumvatu liu lace loti, ‘Bwera kwa Ine.’ Ngana inu simungathe kunena kuti, ‘Ambuye Yesu, ndikudza?’ Nenani kwa Yesu kuti mufuna kuti iye akhale mbusa wanu kuyambira lero. Patsaninso kalatayu kwa munthu wina awerengenso.More from this collection